49 ‘Tamvera! Cholakwa cha m’bale wako Sodomu chinali, kunyada,+ kukhala ndi chakudya chokwanira+ ndiponso kukhala ndi moyo wabata+ ndi wosatekeseka. Izi n’zimene iye ndi midzi yake yozungulira anali nazo.+ Sanalimbitse dzanja la munthu wosautsika+ ndi wosauka.+