1 Samueli 3:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Nyale ya Mulungu inali isanazimitsidwe, ndipo Samueli anali atagona m’kachisi+ wa Yehova, mmene munali likasa la Mulungu. 2 Samueli 22:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,+Ndinaitana Mulungu wanga.+Pamenepo iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake,+Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+ 1 Mbiri 16:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Motero analowetsa+ likasa la Mulungu woona muhema limene Davide anamanga, n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu woona.+ Salimo 11:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu. Yona 2:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pamene ndinalefuka kwambiri,+ ndinakumbukira Yehova.+Ndipo pemphero langa linafika kwa inu, m’kachisi wanu woyera.+
3 Nyale ya Mulungu inali isanazimitsidwe, ndipo Samueli anali atagona m’kachisi+ wa Yehova, mmene munali likasa la Mulungu.
7 Pa nthawi ya zowawa zanga ndinaitana Yehova,+Ndinaitana Mulungu wanga.+Pamenepo iye anamva mawu anga ali m’kachisi wake,+Makutu ake anamva kulira kwanga kopempha thandizo.+
16 Motero analowetsa+ likasa la Mulungu woona muhema limene Davide anamanga, n’kuika likasalo pamalo ake muhemalo.+ Kenako iwo anapereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano kwa Mulungu woona.+
4 Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+Yehova, mpando wake wachifumu uli kumwamba.+Maso ake amaona, maso ake owala amasanthula+ ana a anthu.
7 Pamene ndinalefuka kwambiri,+ ndinakumbukira Yehova.+Ndipo pemphero langa linafika kwa inu, m’kachisi wanu woyera.+