Salimo 140:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Anthu odzikweza anditchera msampha.+Iwo aika zingwe ponseponse ngati ukonde m’mphepete mwa njira,+Ndipo anditchera makhwekhwe.+ [Seʹlah.] Salimo 142:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga+ unalefuka.Pamenepo, munadziwa njira yanga.+Adani anga anditchera msampha+M’njira imene ndikuyenda.+ Yeremiya 18:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 M’nyumba zawo mumveke kulira mukawabweretsera magulu achifwamba mwadzidzidzi,+ chifukwa andikumbira mbuna kuti andigwire ndipo anditchera misampha kuti akole mapazi anga.+ Luka 11:54 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 54 Anali kuyembekezera+ kumva mawu oti amutape nawo m’kamwa.+ Luka 20:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, n’cholinga choti akamukole+ m’mawu ake, kuti akamupereke ku boma ndi kwa bwanamkubwa.+
5 Anthu odzikweza anditchera msampha.+Iwo aika zingwe ponseponse ngati ukonde m’mphepete mwa njira,+Ndipo anditchera makhwekhwe.+ [Seʹlah.]
3 Ndinachita zimenezi pamene mtima wanga+ unalefuka.Pamenepo, munadziwa njira yanga.+Adani anga anditchera msampha+M’njira imene ndikuyenda.+
22 M’nyumba zawo mumveke kulira mukawabweretsera magulu achifwamba mwadzidzidzi,+ chifukwa andikumbira mbuna kuti andigwire ndipo anditchera misampha kuti akole mapazi anga.+
20 Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, n’cholinga choti akamukole+ m’mawu ake, kuti akamupereke ku boma ndi kwa bwanamkubwa.+