Masalimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimbo ya Davide.
140 Inu Yehova, ndilanditseni kwa anthu oipa.+
Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa,+
2 Anthu amene amakonza chiwembu mumtima mwawo,+
Amene amandiukira tsiku lonse ngati mmene zimakhalira pankhondo.+
4 Inu Yehova, ndithandizeni kuti manja a munthu woipa asandikhudze.+
Nditetezeni kwa munthu wochita zachiwawa.+
Nditetezeni kwa anthu amene andikonzera chiwembu kuti andikankhe ndi kundigwetsa.+
5 Anthu odzikweza anditchera msampha.+
Iwo aika zingwe ponseponse ngati ukonde m’mphepete mwa njira,+
Ndipo anditchera makhwekhwe.+ [Seʹlah.]
6 Ndauza Yehova kuti: “Inu ndinu Mulungu wanga.+
Tcherani khutu, inu Yehova, ku mawu anga ochonderera.”+
7 Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa,+ mpulumutsi wanga wamphamvu,+
Mwatchinga ndi kuteteza mutu wanga pa tsiku lankhondo.+
8 Inu Yehova, munthu woipa musam’patse zimene mtima wake umafuna.+
Musalole kuti chiwembu chawo chitheke chifukwa angadzikweze.+ [Seʹlah.]
10 Muwakhuthulire makala oyaka moto pamutu pawo.+
Muwachititse kugwera m’moto+ ndi m’madzi akuya kuti asanyamukenso.+
11 Munthu wolankhula zazikulu* asakhazikike padziko lapansi.+
Zoipa zisakesake munthu wochita zachiwawa ndipo zimukanthe mobwerezabwereza.+