2 Mbiri 6:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 “Anthu anu akakuchimwirani+ (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu n’kuwakwiyira, n’kuwapereka kwa mdani, adani awowo n’kuwagwira kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ Yobu 9:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 “Ndikudziwa bwino kuti zili choncho.Koma kodi munthu angakhale bwanji wosalakwa pa mlandu wotsutsana ndi Mulungu?+ Salimo 51:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Taonani! Anandilandira mu zowawa za pobereka ndili wochimwa.+Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+ Salimo 130:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Inu Ya, mukanakhala kuti mumayang’anitsitsa zolakwa,+Ndani akanaima pamaso panu, inu Yehova?+ Mlaliki 7:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Palibe munthu wolungama padziko lapansi amene amachita zabwino zokhazokha osachimwa.+ Aroma 3:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 monga mmene Malemba amanenera kuti: “Palibe munthu wolungama ndi mmodzi yemwe.+ 1 Yohane 1:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Tikanena kuti: “Sitinachimwe,” ndiye kuti tikumuchititsa iye kukhala wabodza, ndipo mawu ake sali mwa ife.+
36 “Anthu anu akakuchimwirani+ (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu n’kuwakwiyira, n’kuwapereka kwa mdani, adani awowo n’kuwagwira kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+
2 “Ndikudziwa bwino kuti zili choncho.Koma kodi munthu angakhale bwanji wosalakwa pa mlandu wotsutsana ndi Mulungu?+
5 Taonani! Anandilandira mu zowawa za pobereka ndili wochimwa.+Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+
10 Tikanena kuti: “Sitinachimwe,” ndiye kuti tikumuchititsa iye kukhala wabodza, ndipo mawu ake sali mwa ife.+