Yobu 9:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,+Ndiponso zinthu zodabwitsa zosawerengeka.+ Yobu 26:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Komatu zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake,+Ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”+ Yobu 36:26 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 26 Mulungu ndi wokwezeka kuposa mmene tikudziwira.+Zaka zake n’zosawerengeka.+ Salimo 92:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Ntchito zanu ndi zazikuludi inu Yehova!+Maganizo anu ndi ozama kwambiri.+ Salimo 139:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Kwa ine ndi zovuta kwambiri kuti ndidziwe zinthu zonsezi.+Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+ Aroma 11:33 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake?
14 Komatu zimenezi ndi kambali kakang’ono chabe ka zochita zake,+Ndipo timangomva kunong’ona kwapansipansi kwa mawu ake.Koma kodi mabingu ake amphamvu, angawamvetse ndani?”+
6 Kwa ine ndi zovuta kwambiri kuti ndidziwe zinthu zonsezi.+Ndi zapamwamba kwambiri moti sindingathe kuzifikira.+
33 Ndithudi, madalitso amene Mulungu amapereka ndi ochuluka kwambiri.+ Nzeru+ zake n’zozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambiri.+ Ziweruzo zake ndi zosasanthulika,+ ndipo ndani angatulukire njira zake?