45 kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake pa anthu oipa ndi abwino, ndi kuvumbitsira mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+
17 Mphatso iliyonse yabwino+ ndi yangwiro imachokera kumwamba,+ pakuti imatsika kuchokera kwa Atate wa zounikira zonse zakuthambo,+ ndipo iye sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.+