Miyambo 14:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Munthu amene amakwiya msanga amachita zinthu zopusa,+ koma munthu wotha kuganiza bwino amadedwa.+ Miyambo 18:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Milomo ya munthu wopusa imalowa mu mkangano,+ ndipo pakamwa pake pamaitana zikwapu.+ Mlaliki 7:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Usamafulumire kukwiya mumtima mwako,+ pakuti anthu opusa ndi amene sachedwa kupsa mtima.+ Yakobo 4:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Kodi nkhondo zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Nanga kukangana pakati panu kukuchokera kuti? Kodi sizikuchokera m’zilakolako za thupi lanu+ zimene zikuchita nkhondo m’ziwalo zanu?+
4 Kodi nkhondo zimene zikuchitika pakati panu zikuchokera kuti? Nanga kukangana pakati panu kukuchokera kuti? Kodi sizikuchokera m’zilakolako za thupi lanu+ zimene zikuchita nkhondo m’ziwalo zanu?+