Numeri 14:44 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 44 Komabe, anthuwo ananyamuka mwa iwo okha ulendo wopita kudera lamapiri kuja,+ koma likasa la pangano la Yehova silinachoke pakati pa msasa. Mose nayenso sanachoke.+ Esitere 6:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Kenako mfumu inati: “Kodi m’bwalo muli ndani?” Tsopano Hamani anali atalowa m’bwalo lakunja+ kwa nyumba ya mfumu kudzauza mfumu kuti apachike Moredekai pamtengo+ umene anamukonzera. Miyambo 16:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Kunyada kumafikitsa munthu ku chiwonongeko,+ ndipo mtima wodzikuza umachititsa munthu kupunthwa.+ Yakobo 4:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Koma tsopano mumakonda kudzitama.+ Kunyada konse koteroko ndi koipa.
44 Komabe, anthuwo ananyamuka mwa iwo okha ulendo wopita kudera lamapiri kuja,+ koma likasa la pangano la Yehova silinachoke pakati pa msasa. Mose nayenso sanachoke.+
4 Kenako mfumu inati: “Kodi m’bwalo muli ndani?” Tsopano Hamani anali atalowa m’bwalo lakunja+ kwa nyumba ya mfumu kudzauza mfumu kuti apachike Moredekai pamtengo+ umene anamukonzera.