-
Ekisodo 18:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Koma mwa anthu onsewa, usankhe amuna oyenerera,+ oopa Mulungu,+ okhulupirika,+ odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kukhala otsogolera anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+
-
-
Yesaya 33:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 “Pali munthu amene amayenda m’chilungamo nthawi zonse,+ amene amalankhula zowongoka,+ amene amakana kupeza phindu mwachinyengo,+ amene salola kuti manja ake alandire chiphuphu,+ amene amatseka makutu ake kuti asamve nkhani zokhudza kukhetsa magazi, ndiponso amene amatseka maso ake kuti asaone zoipa.+
-