-
Genesis 38:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Tamara atamva zimenezo, anavula zovala zake zaumasiye n’kufunda nsalu. Kenako anaphimba nkhope yake ndi nsalu ina. Atatero anakakhala pansi pachipata cha Enaimu m’mbali mwa msewu wopita ku Timuna. Tamara anachita zimenezi poona kuti Shela wakula, koma apongozi ake sakudzam’tenga kuti akakhale mkazi wa Shelayo.+
-
-
Yeremiya 4:30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 Iwe unali kuvala zovala zamtengo wapatali,* unali kudzikongoletsa ndi zokongoletsera zagolide ndipo unali kudzikongoletsa m’maso mwako ndi utoto wakuda.+ Tsopano utani popeza wafunkhidwa? Unali kutaya nthawi ndi kudzikongoletsa.+ Amene anali kukukhumba tsopano akukukana ndipo akufunafuna moyo wako.+
-