Miyambo 12:18 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 18 Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga,+ koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.+ Miyambo 16:24 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 24 Mawu okoma ali ngati chisa cha uchi.+ Amakhala okoma kwa munthu ndipo amachiritsa mafupa.+ Miyambo 17:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Aliyense wosalankhulapo mawu ake ndi wodziwa zinthu,+ ndipo munthu wozindikira amakhala wofatsa.+
18 Pali munthu amene amalankhula mosaganizira ndi mawu olasa ngati lupanga,+ koma lilime la anthu anzeru limachiritsa.+