-
Yesaya 1:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Yehova wanena kuti: “Kodi nsembe zanu zambirimbirizo zili ndi phindu lanji kwa ine? Nsembe zopsereza zathunthu+ za nkhosa zamphongo+ ndiponso mafuta a nyama zodyetsedwa bwino zandikwana.+ Ine sindikusangalalanso+ ndi magazi+ a ana a ng’ombe amphongo, ana a nkhosa amphongo ndiponso a mbuzi zamphongo.+
-
-
Yesaya 66:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 “Munthu amene akupha ng’ombe yamphongo ali ngati wopha munthu.+ Amene akupereka nsembe ya nkhosa ali ngati wothyola khosi la galu.+ Wopereka mphatso ali ngati wopereka magazi a nkhumba.+ Wopereka lubani wachikumbutso+ ali ngati wopereka dalitso pogwiritsa ntchito mawu onenerera zamatsenga.+ Anthuwo asankha njira zawozawo, ndipo amasangalala ndi zinthu zawo zonyansa.+
-