Salimo 69:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Mtima wanga wasweka chifukwa cha chitonzo, ndipo chilonda chake ndi chosachiritsika.+Ndinali kuyembekezera kuti wina andimvere chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+Ndinali kuyembekezera onditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+ Salimo 142:4 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 4 Yang’anani kudzanja lamanja ndipo muoneKuti palibe aliyense amene akufuna kundithandiza.+Ndilibenso malo othawirako,+Ndipo palibe amene akufunsa za moyo wanga.+ 2 Timoteyo 4:16 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 16 Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha.+ Ngakhale zinali choncho, usakhale mlandu kwa iwo.+
20 Mtima wanga wasweka chifukwa cha chitonzo, ndipo chilonda chake ndi chosachiritsika.+Ndinali kuyembekezera kuti wina andimvere chifundo, koma panalibe ndi mmodzi yemwe,+Ndinali kuyembekezera onditonthoza, koma sanapezeke ngakhale mmodzi.+
4 Yang’anani kudzanja lamanja ndipo muoneKuti palibe aliyense amene akufuna kundithandiza.+Ndilibenso malo othawirako,+Ndipo palibe amene akufunsa za moyo wanga.+
16 Pamene ndinali kudziteteza koyamba pa mlandu wanga, palibe amene anakhala kumbali yanga. Onse anandisiya ndekha.+ Ngakhale zinali choncho, usakhale mlandu kwa iwo.+