Aroma 5:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Si zokhazo, koma tiyeni tikondwere pamene tili m’masautso,+ popeza tikudziwa kuti chisautso chimabala chipiriro.+ 2 Akorinto 4:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Pakuti ngakhale kuti masautso amene tikukumana nawo ndi akanthawi+ ndipo ndi opepuka, masautsowo akutichititsa kuti tilandire ulemerero umene ukukulirakulira komanso wamuyaya,+ 2 Akorinto 7:10 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 10 Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa ndi kupeza chipulumutso, zimene munthu sangadandaule nazo.+ Koma chisoni cha dziko chimabweretsa imfa.+ Aheberi 12:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+
3 Si zokhazo, koma tiyeni tikondwere pamene tili m’masautso,+ popeza tikudziwa kuti chisautso chimabala chipiriro.+
17 Pakuti ngakhale kuti masautso amene tikukumana nawo ndi akanthawi+ ndipo ndi opepuka, masautsowo akutichititsa kuti tilandire ulemerero umene ukukulirakulira komanso wamuyaya,+
10 Kumva chisoni mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu kumachititsa munthu kulapa ndi kupeza chipulumutso, zimene munthu sangadandaule nazo.+ Koma chisoni cha dziko chimabweretsa imfa.+
11 Zoonadi, palibe chilango chimene chimamveka chosangalatsa pa nthawi yomwe ukuchilandira, koma chimakhala chowawa.+ Komabe pambuyo pake, kwa anthu amene aphunzirapo kanthu pa chilangocho, chimabala chipatso chamtendere,+ chomwe ndi chilungamo.+