Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 18:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Ukudalira thandizo la Iguputo,+ bango lophwanyika+ loti munthu ataligwira kuti limuchirikize, lingamucheke m’manja. Umu ndi mmene Farao+ mfumu ya Iguputo alili kwa onse omudalira.

  • Yesaya 31:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Tsoka kwa anthu amene akupita ku Iguputo kukapempha thandizo.+ Iwo akudalira mahatchi wamba+ ndi kukhulupirira magaleta ankhondo,+ chifukwa chakuti ndi ambiri. Akudaliranso mahatchi akuluakulu chifukwa chakuti ndi amphamvu kwambiri, koma sanayang’ane kwa Woyera wa Isiraeli ndipo sanafunefune Yehova.+

  • Yesaya 31:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Koma Aiguputowo ndi anthu ochokera kufumbi.+ Si Mulungu ayi. Mahatchi awo ndi zinyama,+ osati mzimu. Yehova akadzatambasula dzanja lake, amene akupereka thandizo adzapunthwa, ndipo amene akuthandizidwawo adzagwa.+ Onsewo adzatha nthawi imodzi.

  • Yeremiya 43:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Nebukadirezara adzabwera kudzathira nkhondo dziko la Iguputo.+ Woyenera kufa ndi mliri adzafa ndi mliri. Woyenera kutengedwa kupita ku ukapolo adzatengedwa kupita ku ukapolo. Woyenera kufa ndi lupanga adzafa ndi lupanga.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena