-
Yesaya 9:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 N’chifukwa chake Yehova sadzasangalalira ngakhale anyamata awo,+ ndipo sadzamvera chisoni ana awo amasiye* ndi akazi awo amasiye, pakuti onsewo ndi opanduka+ ndi ochita zoipa ndipo pakamwa paliponse pakulankhula zopanda nzeru. Chifukwa cha zonsezi, mkwiyo wake sunabwerere, ndipo dzanja lake lidakali lotambasula.+
-
-
Yesaya 32:6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 pakuti munthu wopusa adzalankhula zinthu zopanda nzeru,+ ndipo mtima wake udzaganiza zochita zinthu zopweteka ena.+ Iye adzachita zimenezi kuti azichita zopanduka,+ kuti azinenera Yehova zoipa, kuti achititse mimba ya munthu wanjala kukhala yopanda kanthu,+ ndiponso kuti achititse munthu waludzu kukhala wopanda chilichonse choti amwe.
-