3 Inu Yehova, kodi maso anu sakulakalaka kuona munthu wokhulupirika?+ Mwawalanga+ koma sanamve kupweteka.+ Ngakhale kuti munatsala pang’ono kuwafafaniza onse,+ iwo sanaphunzirepo kanthu.+ Anaumitsa nkhope zawo ngati thanthwe.+ Ndipo anakana kubwerera kwa inu.+