Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yoswa 21:45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 45 Palibe lonjezo ngakhale limodzi limene silinakwaniritsidwe, pa malonjezo onse abwino amene Yehova analonjeza nyumba ya Isiraeli. Onse anakwaniritsidwa.+

  • Yoswa 23:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 “Tsopano taonani! Ine ndatsala pang’ono kufa.+ Inu mukudziwa bwino ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse, kuti pamawu onse abwino amene Yehova Mulungu wanu ananena kwa inu, palibe ngakhale amodzi omwe sanakwaniritsidwe. Onse akwaniritsidwa kwa inu. Palibe ngakhale mawu amodzi omwe sanakwaniritsidwe.+

  • Yesaya 55:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 ndi mmenenso adzakhalire mawu otuluka pakamwa panga.+ Sadzabwerera kwa ine popanda kukwaniritsa cholinga chake,+ koma adzachitadi zimene ine ndikufuna+ ndipo adzakwaniritsadi zimene ndinawatumizira.+

  • Zekariya 1:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Kodi zimene ndinalamula atumiki anga aneneri+ m’mawu anga ndi m’malangizo anga, sizinawachitikire makolo anu?’+ Chotero iwo anabwerera kwa ine ndi kunena kuti: ‘Yehova wa makamu watichitira zimene anakonza kuti atichitire+ mogwirizana ndi njira zathu ndi zochita zathu.’”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena