10 Anthu owomboledwa ndi Yehova adzabwerera+ n’kukafika ku Ziyoni akufuula mosangalala.+ Iwo azidzasangalala mpaka kalekale.+ Adzakhala okondwa ndi osangalala ndipo chisoni ndi kubuula zidzachoka.+
10 Ndidzawabweretsa kuchokera kudziko la Iguputo.+ Ndidzawasonkhanitsa pamodzi kuchokera ku Asuri.+ Ndidzawabweretsa kudera la Giliyadi+ ndi la Lebanoni chifukwa chakuti malo okwanira anthu onsewo sadzapezeka.+
31 Iye adzatumiza angelo ake ndi kulira kwamphamvu kwa lipenga,+ ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake+ kuchokera kumphepo zinayi,+ kuchokera kumalekezero a m’mlengalenga mpaka kumalekezero ena.