Mateyu 8:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Anachita izi kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: “Iye anatenga matenda athu n’kunyamula zowawa zathu.”+ Mateyu 9:2 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 2 Kumeneko anthu anam’bweretsera munthu wakufa ziwalo, atagona pakabedi.+ Poona chikhulupiriro chawo, Yesu anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Limba mtima, mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+ Mateyu 9:20 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 20 Tsopano mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi kwa zaka 12+ anafika kumbuyo kwake n’kugwira ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake akunja,+ Mateyu 9:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Tsopano pamene iwo anali kunyamuka, anthu anam’bweretsera munthu wosalankhula wogwidwa ndi chiwanda.+ Luka 5:31 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 31 Poyankha, Yesu anawauza kuti: “Anthu athanzi safuna dokotala,+ koma odwala ndi amene amamufuna.+
17 Anachita izi kuti zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya zikwaniritsidwe. Iye ananena kuti: “Iye anatenga matenda athu n’kunyamula zowawa zathu.”+
2 Kumeneko anthu anam’bweretsera munthu wakufa ziwalo, atagona pakabedi.+ Poona chikhulupiriro chawo, Yesu anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Limba mtima, mwanawe, machimo ako akhululukidwa.”+
20 Tsopano mayi wina amene anali ndi nthenda yotaya magazi kwa zaka 12+ anafika kumbuyo kwake n’kugwira ulusi wopota wa m’mphepete mwa malaya ake akunja,+
32 Tsopano pamene iwo anali kunyamuka, anthu anam’bweretsera munthu wosalankhula wogwidwa ndi chiwanda.+