25 Koma Yehova wanena kuti: “Ngakhale gulu la anthu ogwidwa ndi munthu wamphamvu lidzatengedwa,+ ndipo amene anatengedwa kale ndi wolamulira wankhanza adzathawa.+ Aliyense wolimbana nawe, ineyo ndidzalimbana naye,+ ndipo ana ako ndidzawapulumutsa.+
44 “M’masiku a mafumu amenewo,+ Mulungu wakumwamba+ adzakhazikitsa ufumu+ umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.+ Ufumuwo sudzaperekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu,+ koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo,+ ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.+
18 Ukatsegule maso awo,+ kuwachotsa mu mdima+ ndi kuwatembenuzira ku kuwala.+ Kuwachotsa m’manja mwa Satana+ ndi kuwatembenuzira kwa Mulungu, kuti machimo awo akhululukidwe+ ndi kukalandira cholowa+ pamodzi ndi oyeretsedwa,+ mwa chikhulupiriro chawo mwa ine.’