10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi wozindikira zinsinsi zopatulika za ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawo, zonse ndi mafanizo okhaokha.+ Izi zili choncho kuti kuona aziona ndithu, koma kukhale kopanda phindu, kumvanso azimva ndithu, koma asazindikire tanthauzo lake.+