25 Anagwiranso akalonga awiri a Amidiyani, Orebi ndi Zeebi.+ Atatero, anapha Orebi pathanthwe la Orebi,+ ndipo Zeebi anamuphera pamalo opondera mphesa a Zeebi. Iwo anapitirizabe kuthamangitsa Amidiyani,+ kenako anabweretsa mutu wa Orebi ndi Zeebi kwa Gidiyoni m’chigawo cha Yorodano.+