Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 13:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Nyama zam’tchire zokhala kumadera opanda madzi zidzagona kumeneko, ndipo nyumba za anthu amene anali kukhala kumeneko zidzadzaza ndi akadzidzi.+ Nthiwatiwa zizidzakhala kumeneko, ndipo ziwanda zooneka ngati mbuzi* zizidzadumphadumpha kumeneko.+

  • Yeremiya 50:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Choncho nyama za m’madera opanda madzi, nyama zokonda kulira mokuwa ndi nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Simudzakhalanso munthu mmenemo ndipo mzindawo sudzapezekanso ku mibadwomibadwo.”+

  • Yeremiya 51:25
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 “Ine ndikuthira nkhondo iwe+ phiri lowononga,+ amene wawononga dziko lonse lapansi.+ Ndidzatambasula dzanja langa ndi kukuthira nkhondo. Ndidzakugubuduza kukuchotsa pamatanthwe ndipo ndidzakusandutsa phiri lotenthedwa ndi moto,” watero Yehova.+

  • Yeremiya 51:62
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 62 Ukanene kuti, ‘Inu Yehova! Inu mwanena zowononga malo ano ndi kuwafafaniza kuti pasapezekenso chilichonse chokhalamo.+ Musapezeke munthu kapena chiweto koma mzindawo ukhale bwinja mpaka kalekale.’

  • Chivumbulutso 18:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Iye anafuula ndi mawu amphamvu,+ akuti: “Wagwa! Babulo Wamkulu wagwa,+ ndipo wakhala malo okhala ziwanda, ndiponso obisalamo mpweya+ uliwonse wonyansa wotuluka m’kamwa, komanso obisalamo mbalame iliyonse yonyansa ndi yodedwa.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena