Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 13:20
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 M’Babulo simudzakhalanso anthu,+ ndipo iye sadzakhalaponso ku mibadwomibadwo.+ Kumeneko Mluya sadzakhomako hema wake, ndipo abusa sadzagonekako ziweto zawo.

  • Yesaya 14:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 “Babulo ndidzamusandutsa malo okhala nungu* ndiponso malo a zithaphwi. Ndidzamusesa ndi tsache* la chiwonongeko,”+ watero Yehova wa makamu.

  • Yeremiya 50:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 3 Pakuti mtundu wina wabwera kudzamuukira kuchokera kumpoto.+ Umenewu ndi mtundu umene wasandutsa dziko lake kukhala chinthu chodabwitsa, moti m’dzikoli mulibe aliyense wokhalamo.+ Anthu ndiponso ziweto zathawa.+ Zonse zapita.”+

  • Yeremiya 50:39
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 39 Choncho nyama za m’madera opanda madzi, nyama zokonda kulira mokuwa ndi nthiwatiwa zidzakhala mmenemo.+ Simudzakhalanso munthu mmenemo ndipo mzindawo sudzapezekanso ku mibadwomibadwo.”+

  • Yeremiya 51:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Dziko ligwedezeke ndi kumva ululu waukulu,+ chifukwa Yehova waganiza zokhaulitsa Babulo kuti dzikolo likhale chinthu chodabwitsa, lopanda munthu wokhalamo.+

  • Yeremiya 51:37
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 37 Babulo adzakhala milu yamiyala+ ndi malo obisalamo mimbulu.+ Adzakhala chinthu chodabwitsa ndi chochiimbira mluzu ndipo simudzapezeka munthu wokhalamo.+

  • Chivumbulutso 18:23
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 23 Kuwala kwa nyale sikudzaunikanso mwa iwe. Mawu a mkwati ndi a mkwatibwi sadzamvekanso+ mwa iwe, chifukwa amalonda ako oyendayenda+ anali anthu apamwamba+ padziko lapansi, ndiponso mitundu yonse ya anthu inasocheretsedwa ndi zochita zako zamizimu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena