Numeri 22:41 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 41 M’mawa kutacha, Balaki anakatenga Balamu n’kupita naye ku Bamoti-baala.+ Anam’tengera kumeneko kuti akathe kuliona bwino khamu lonse la Aisiraeli.+ Numeri 23:1 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Tsopano Balamu anauza Balaki kuti: “Mundimangire pamalo ano maguwa ansembe+ okwanira 7. Mukatero mundikonzere ng’ombe zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.” Yeremiya 48:35 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 35 Ndidzachititsa kuti m’dziko la Mowabu musapezeke aliyense wobweretsa nsembe kumalo okwezeka komanso wofukiza nsembe yautsi kwa mulungu wake,’+ watero Yehova.
41 M’mawa kutacha, Balaki anakatenga Balamu n’kupita naye ku Bamoti-baala.+ Anam’tengera kumeneko kuti akathe kuliona bwino khamu lonse la Aisiraeli.+
23 Tsopano Balamu anauza Balaki kuti: “Mundimangire pamalo ano maguwa ansembe+ okwanira 7. Mukatero mundikonzere ng’ombe zamphongo 7, ndi nkhosa zamphongo 7.”
35 Ndidzachititsa kuti m’dziko la Mowabu musapezeke aliyense wobweretsa nsembe kumalo okwezeka komanso wofukiza nsembe yautsi kwa mulungu wake,’+ watero Yehova.