16 Yehova adzabangula ngati mkango kuchokera m’Ziyoni ndipo adzalankhula ali ku Yerusalemu.+ Kumwamba ndi dziko lapansi zidzagwedezeka+ koma Yehova adzakhala chitetezo kwa anthu ake,+ ndipo adzakhala malo a chitetezo champhamvu kwa ana a Isiraeli.+
“Yehova adzabangula ngati mkango mu Ziyoni,+ ndipo adzafuula mu Yerusalemu.+ Malo amene abusa amadyetserako ziweto adzalira, ndipo pansonga ya phiri la Karimeli padzauma.”+