10 Tsopano Baruki anayamba kuwerenga mpukutuwo mokweza pamaso pa anthu onse. Anayamba kuwerenga mawu onse a Yeremiya panyumba ya Yehova. Anachita izi m’chipinda chodyera+ cha Gemariya+ mwana wa Safani+ wokopera Malemba,+ m’bwalo lakumtunda, pakhomo la chipata chatsopano cha nyumba ya Yehova.+