-
2 Mafumu 24:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mfumuyo inatenga+ anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ amuna onse amphamvu ndi olimba mtima,+ mmisiri aliyense+ ndi munthu aliyense womanga makoma achitetezo, n’kupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu onyozeka+ okha a m’dzikolo.
-
-
Yeremiya 24:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Ndiyeno Yehova anandisonyeza madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandisonyeza zimenezi Nebukadirezara mfumu ya Babulo atatenga Yekoniya+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri+ ndi omanga makoma achitetezo kuchokera ku Yerusalemu kupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+
-