26 Anthu adzabwera kuchokera m’mizinda ya Yuda, m’madera ozungulira Yerusalemu, m’dziko la Benjamini,+ kuchigwa,+ m’dera lamapiri+ komanso kuchokera kum’mwera.+ Iwo adzabweretsa kunyumba ya Yehova nsembe zopsereza zathunthu,+ nsembe zina,+ nsembe zambewu,+ lubani+ ndi nsembe zoyamikira.+