Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 1 Samueli 8:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Zinthu zonse zimene akhala akuchita kuyambira pa tsiku limene ndinawatulutsa mu Iguputo+ mpaka lero, kundisiya+ n’kumakatumikira milungu ina,+ n’zimenenso akuchitira iwe.

  • 2 Mafumu 17:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Koma iwo sanamvere. M’malomwake anaumitsa makosi awo,+ ngati mmene makolo awo anaumitsira makosi awo. Makolo awowo sanasonyeze chikhulupiriro+ mwa Yehova Mulungu wawo.

  • Nehemiya 9:29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 29 Ngakhale kuti munali kuwalimbikitsa+ kuti abwerere ku chilamulo chanu,+ iwo anali kuchita zinthu modzikuza+ ndipo sanali kumva malamulo anu. Anachimwira zigamulo zanu,+ zimene ngati munthu azitsatira adzakhala ndi moyo chifukwa cha zigamulozo.+ Iwo anatseka makutu*+ awo ndi kuumitsa khosi+ lawo ndipo sanamvere.+

  • Yeremiya 7:26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 26 Koma iwo sanandimvere kapena kutchera khutu lawo.+ M’malomwake anapitiriza kuumitsa khosi lawo,+ ndipo anachita zinthu zoipa kuposa makolo awo.+

  • Zekariya 7:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Iwo anaumitsa mtima wawo+ ngati mwala wolimba kwambiri kuti asamvere malamulo+ ndi mawu a Yehova wa makamu, amene anawatumizira mwa mzimu wake+ kudzera mwa aneneri akale.+ Choncho Yehova wa makamu anakwiya kwambiri.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena