2 Pa nthawi imeneyo, magulu ankhondo a mfumu ya Babulo anali atazungulira Yerusalemu.+ Ndipo mneneri Yeremiya anali atamutsekera m’nyumba imene inali m’Bwalo la Alonda.+ Bwalo limeneli linali pafupi ndi nyumba ya mfumu ya Yuda.
15 Pamenepo akalonga+ anamukwiyira kwambiri Yeremiya+ ndipo anamumenya+ ndi kumutsekera m’ndende+ m’nyumba ya Yehonatani+ mlembi, pakuti nyumba yake ndi imene anaisandutsa ndende.+