19 Iyo inatentha nyumba ya Mulungu woona+ ndi kugwetsa mpanda+ wa Yerusalemu. Ababulowo anatenthanso ndi moto nyumba zonse zokhala ndi mipanda yolimba kwambiri za mzindawo ndi zinthu zake zonse zabwinozabwino,+ mpaka zonse zinawonongedwa.+
18 Koma ngati simudzadzipereka kwa akalonga a mfumu ya Babulo, ndiye kuti mzinda uno udzaperekedwa m’manja mwa Akasidi ndipo adzautentha.+ Inuyo simudzapulumuka m’manja mwawo.’”+