22 Ndiyeno Mfumu Asa inaitanitsa Ayuda onse,+ moti palibe amene sanaitanidwe, ndipo iwo anatenga miyala ya ku Rama ndi matabwa ake, zimene Basa ankamangira. Mfumu Asa inatenga zinthu zimenezo n’kuyamba kukamangira mzinda wa Geba+ ku Benjamini, ndi mzinda wa Mizipa.+