Yeremiya 5:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 “Iwo akana Yehova, ndipo akunena kuti, ‘Iye kulibe.+ Ndipo ife tsoka silidzatigwera. Sitidzaona lupanga lililonse kapena njala yaikulu.’+ Yeremiya 6:14 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa anthu anga ponena kuti, ‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.+ Yeremiya 14:13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 13 Pamenepo ndinati: “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Lupanga silidzakukanthani, ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni m’malo ano.’”+ Yeremiya 23:17 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+ 1 Atesalonika 5:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Pamene azidzati:+ “Bata ndi mtendere!”+ chiwonongeko+ chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati,+ ndipo sadzapulumuka.+
12 “Iwo akana Yehova, ndipo akunena kuti, ‘Iye kulibe.+ Ndipo ife tsoka silidzatigwera. Sitidzaona lupanga lililonse kapena njala yaikulu.’+
14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa anthu anga ponena kuti, ‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.+
13 Pamenepo ndinati: “Kalanga ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Lupanga silidzakukanthani, ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni m’malo ano.’”+
17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+
3 Pamene azidzati:+ “Bata ndi mtendere!”+ chiwonongeko+ chodzidzimutsa chidzafika pa iwo nthawi yomweyo monga zowawa za pobereka za mkazi wapakati,+ ndipo sadzapulumuka.+