Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 4:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Pamenepo ndinanena kuti: “Kalanga ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Kunena zoona, mwapusitsa anthu awa+ ndiponso Yerusalemu mwa kunena kuti, ‘Mudzakhala pa mtendere,’+ koma lupanga lawabaya* mpaka mumtima.”

  • Yeremiya 5:31
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 31 Aneneri akulosera monama,+ ndipo ansembe akupondereza anthu ndi mphamvu zawo.+ Anthu anga nawonso akukonda zimenezi.+ Ndipo kodi anthu inu mudzachita chiyani pamapeto pake?”+

  • Yeremiya 6:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo+ kuwonongeka kwa anthu anga ponena kuti, ‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’ pamene kulibe mtendere.+

  • Yeremiya 23:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Anthu inu mudzakhala pa mtendere.”’+ Ndipo aliyense woumitsa mtima wake+ akumuuza kuti, ‘Tsoka silidzakugwerani anthu inu.’+

  • Yeremiya 27:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 “‘“‘Anthu inu musamvere aneneri,+ ochita zamaula, olota maloto,+ ochita zamatsenga ndi obwebweta+ amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Anthu inu simudzatumikira mfumu ya Babulo.”+

  • Ezekieli 13:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 chifukwa chakuti iwo asocheretsa anthu anga ponena kuti, “Tili pa mtendere!” Koma palibe mtendere.+ Palinso munthu amene akumanga khoma lachipinda, ndipo anthu ena akulipaka laimu pachabe.’+

  • Mika 3:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Atsogoleri a mumzindawo saweruza asanalandire chiphuphu+ ndipo ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro.+ Aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+ Komatu iwo amadalira Yehova ndipo amanena kuti: “Kodi Yehova sali pakati pathu?+ Choncho tsoka silidzatigwera.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena