12 Koma mwamuna wake akafafaniza malonjezowo pa tsiku limene wamva mawu alionse otuluka pakamwa pa mkaziyo, mawu olonjezerawo kapena malonjezo ake odzimana amene walumbirira moyo wake, malonjezo a mkaziyo akhale opanda ntchito.+ Mwamuna wake wawafafaniza, ndipo Yehova adzam’khululukira mkaziyo.+