21 Ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda+ ndi akalonga ake ndidzawapereka m’manja mwa adani awo, m’manja mwa anthu ofuna moyo wawo ndiponso m’manja mwa magulu ankhondo a mfumu ya ku Babulo+ amene akubwerera osakuthirani nkhondo.’+
5 Pamenepo gulu lankhondo la Akasidi linawathamangitsa+ ndipo Zedekiya anamupeza m’chipululu cha Yeriko.+ Atamugwira, anamutenga ndi kupita naye kwa Nebukadirezara mfumu ya Babulo ku Ribila,+ m’dziko la Hamati,+ kuti Nebukadirezara akamuweruze.+