Yobu 40:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Uone wodzikweza aliyense n’kumuchepetsa,+Ndipo oipa uwaponderezere pamalo pomwe alilipo. Miyambo 18:12 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Munthu asanagwe, mtima wake umadzikweza,+ ndipo asanapeze ulemerero, amadzichepetsa.+ Yesaya 25:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Iye adzatambasula manja ake n’kuwamenyetsa pakati pa mzindawo ngati mmene munthu wosambira amatambasulira manja ake n’kuwamenyetsa pamadzi akamasambira. Adzathetsa kunyada+ kwa mzindawo poumenya mwaluso ndi manja ake. Yakobo 4:6 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+
11 Iye adzatambasula manja ake n’kuwamenyetsa pakati pa mzindawo ngati mmene munthu wosambira amatambasulira manja ake n’kuwamenyetsa pamadzi akamasambira. Adzathetsa kunyada+ kwa mzindawo poumenya mwaluso ndi manja ake.
6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+