2 Samueli 22:28 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 28 Anthu odzichepetsa mudzawapulumutsa.+Koma mumatsutsa odzikweza, kuti muwatsitse.+ Salimo 18:27 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 27 Chifukwa anthu osautsika mudzawapulumutsa,+Koma anthu odzikweza mudzawatsitsa.+ Miyambo 15:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Yehova adzagwetsa nyumba za anthu odzikuza,+ koma adzakhazikitsa malire a malo a mkazi wamasiye.+ Yesaya 2:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Maso odzikuza a munthu wochokera kufumbi adzatsika, ndipo anthu odzikweza adzawerama.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+ Danieli 4:37 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 37 “Tsopano ine Nebukadinezara ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba,+ chifukwa ntchito zake zonse ndizo choonadi, njira zake ndi zolungama,+ ndiponso amatha kutsitsa anthu onyada.”+
11 Maso odzikuza a munthu wochokera kufumbi adzatsika, ndipo anthu odzikweza adzawerama.+ Yehova yekha ndi amene adzakwezedwe pamwamba m’tsiku limenelo.+
37 “Tsopano ine Nebukadinezara ndikutamanda, kukweza ndi kulemekeza Mfumu yakumwamba,+ chifukwa ntchito zake zonse ndizo choonadi, njira zake ndi zolungama,+ ndiponso amatha kutsitsa anthu onyada.”+