Yesaya 24:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Mwezi wathunthu wachita manyazi. Dzuwa lowala lachitanso manyazi,+ pakuti Yehova wa makamu wakhala mfumu+ yaulemerero m’phiri la Ziyoni+ ndi mu Yerusalemu, pamaso pa anthu ake achikulire.+ Mika 4:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Anthu amene anali kuyenda motsimphina ndidzawasonkhanitsanso pamodzi monga anthu otsala.+ Anthu amene anawachotsa m’dziko lawo ndi kuwapititsa kutali ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+ Yehova adzawalamulira monga mfumu m’phiri la Ziyoni kuyambira nthawi imeneyo mpaka kalekale.+ Zefaniya 2:11 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 11 Yehova adzawachititsa mantha,+ pakuti adzawondetsa milungu yonse ya padziko lapansi.+ Pamenepo anthu adzamugwadira,+ aliyense pamalo pake, zilumba zonse za mitundu ya anthu zidzamugwadira.+
23 Mwezi wathunthu wachita manyazi. Dzuwa lowala lachitanso manyazi,+ pakuti Yehova wa makamu wakhala mfumu+ yaulemerero m’phiri la Ziyoni+ ndi mu Yerusalemu, pamaso pa anthu ake achikulire.+
7 Anthu amene anali kuyenda motsimphina ndidzawasonkhanitsanso pamodzi monga anthu otsala.+ Anthu amene anawachotsa m’dziko lawo ndi kuwapititsa kutali ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+ Yehova adzawalamulira monga mfumu m’phiri la Ziyoni kuyambira nthawi imeneyo mpaka kalekale.+
11 Yehova adzawachititsa mantha,+ pakuti adzawondetsa milungu yonse ya padziko lapansi.+ Pamenepo anthu adzamugwadira,+ aliyense pamalo pake, zilumba zonse za mitundu ya anthu zidzamugwadira.+