Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yeremiya 50:32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Pa tsiku limenelo Babulo Wodzikuza ameneyu adzapunthwa ndi kugwa+ ndipo sipadzapezeka wina womudzutsa.+ Mizinda imene iye amalamulira ndidzaiyatsa moto, ndipo motowo udzawononganso madera onse ozungulira mizindayo.”+

  • Malaki 4:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 4 “Taonani! Tsiku loyaka ngati ng’anjo likubwera,+ ndipo anthu onse odzikuza ndi onse ochita zoipa adzakhala ngati mapesi.+ Tsiku limene likubweralo lidzawanyeketsa moti pa iwo sipadzatsala mizu kapena nthambi,”+ watero Yehova wa makamu.

  • Luka 18:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Ndithu ndikukuuzani, Munthu ameneyu anapita kwawo ataonedwa kukhala wolungama kwambiri+ kusiyana ndi wina uja, chifukwa aliyense wodzikweza adzam’nyazitsa, koma wodzichepetsa adzamukweza.”+

  • Yakobo 4:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Komabe, kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu amapereka kumaposa khalidwe limeneli.+ N’chifukwa chake lemba limati: “Mulungu amatsutsa odzikweza,+ koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.”+

  • 1 Petulo 5:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 Chimodzimodzinso inu anyamata. Muzigonjera+ amuna achikulire. Koma nonsenu muzichitirana zinthu modzichepetsa,+ chifukwa Mulungu amatsutsa odzikweza, koma odzichepetsa amawasonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena