7 Koma Yehova anauza Samueli kuti: “Usaone maonekedwe ake ndi kutalika kwa msinkhu wake,+ pakuti ine ndamukana ameneyu. Chifukwa mmene munthu amaonera si mmene Mulungu amaonera.+ Munthu amaona zooneka ndi maso,+ koma Yehova amaona mmene mtima ulili.”+
31 Ndani mwa ana awiriwa amene anachita chifuniro cha bambo ake?”+ Iwo anati: “Wachiwiriyu.” Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti okhometsa msonkho ndi mahule akukusiyani m’mbuyo n’kukalowa mu ufumu wa Mulungu.