12 Kwezerani mpanda wa Babulo mtengo wa chizindikiro.+ Wonjezerani alonda+ ndipo ikani alondawo pamalo awo. Konzekeretsani omenya nkhondo mobisalira anzawo.+ Pakuti Yehova waganiza zoti achite ndipo adzachitira anthu okhala ku Babulo zimene wanena.”+