8 “Yehova, Mulungu wa makamu, wanena kuti: ‘Ine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ndalumbira pa dzina langa kuti,+ “Ndikunyasidwa ndiponso ndikudana ndi kunyada kwa Yakobo+ ndi nsanja zake zokhalamo,+ chotero ndidzapereka mzindawu ndi zinthu zake zonse kwa adani ake.+