Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 31:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Tsopano Yehova anauza Mose kuti: “Iweyo ugona pamodzi ndi makolo ako,+ ndipo anthu awa adzaimirira+ ndi kuchita chiwerewere pakati pawo ndi milungu yachilendo ya m’dziko limene akupita.+ Iwo adzandisiya+ ndi kuphwanya pangano limene ndinapangana nawo.+

  • 2 Mafumu 17:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Zimenezi zinachitika chifukwa chakuti ana a Isiraeli anachimwira+ Yehova Mulungu wawo, yemwe anawatulutsa m’dziko la Iguputo+ n’kuwachotsa m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, ndipo anayamba kuopa milungu ina.+

  • Ezekieli 16:59
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 59 “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Inenso ndidzakubwezera mogwirizana ndi zochita zako,+ chifukwa unanyoza lumbiro pophwanya pangano langa.+

  • Hoseya 6:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 7 Koma iwo, mofanana ndi munthu wochokera kufumbi, aphwanya pangano.+ Andichitira zachinyengo kumalo kumene amakhala.+

  • Aheberi 8:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 ‘Koma pangano+ limeneli si lofanana ndi limene ndinapangana ndi makolo awo pamene ndinagwira dzanja lawo kuti ndiwatulutse m’dziko la Iguputo,+ chifukwa iwo sanapitirize kusunga pangano+ langalo moti ndinasiya kuwasamalira,’ watero Yehova.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena