Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Salimo 75:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 M’dzanja la Yehova muli kapu.+

      Kapuyo yadzaza ndi vinyo wosakaniza ndi zokometsera ndipo akuchita thovu.

      Ndithudi, iye adzatsanula vinyo yense amene ali m’kapuyo kuphatikizapo nsenga zake.

      Anthu onse oipa padziko lapansi adzamwa ndi kugugudiza nsengazo.”+

  • Yesaya 29:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 9 Anthu inu, dabwani ndipo chitani kukamwa yasa!+ Matani maso anu kuti musaone.+ Iwo aledzera,+ koma osati ndi vinyo. Akudzandira, koma osati chifukwa cha chakumwa choledzeretsa.+

  • Yesaya 51:17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 17 “Dzuka! Dzuka! Imirira iwe Yerusalemu,+ iwe amene wamwa chikho cha mkwiyo wa Yehova kuchokera m’dzanja lake.+ Iweyo wamwa ndipo wagugudiza chipanda, chikho chochititsa munthu kuyenda dzandidzandi.+

  • Yesaya 63:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Ndinapondaponda mitundu ya anthu mu mkwiyo wanga, ndipo ndinawaledzeretsa ndi ukali wanga.+ Ndinachititsa kuti magazi awo atuluke mwamphamvu n’kutayikira pansi.”+

  • Yeremiya 25:27
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 27 “Ndiyeno ukawauze kuti, ‘Yehova wa makamu, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Imwani, muledzere, musanze ndi kugwa osadzukanso+ chifukwa cha lupanga limene ndikukutumizirani pakati panu.”’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena