12 Patapita nthawi, Yehoyakini mfumu ya Yuda anatuluka n’kupita kwa mfumu ya Babulo+ pamodzi ndi mayi ake,+ atumiki ake, akalonga ake, ndi nduna za panyumba yake, ndipo mfumu ya Babuloyo inam’tengera Yehoyakini ku ukapolo m’chaka cha 8+ cha ufumu wake.