Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Deuteronomo 28:65
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 65 Pakati pa mitundu imeneyo sudzakhala mwamtendere,+ ndipo sudzapeza malo oti phazi lako liponde kuti lipumulirepo. Kumeneko, Yehova adzakupatsa mtima wachinthenthe,+ adzachititsa maso ako+ khungu ndipo adzakutayitsa mtima.

  • Yobu 17:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Chifukwa cha kuzunzika, diso langa layamba kuchita mdima.+

      Ziwalo zanga zonse zakhala ngati mthunzi.

  • Salimo 6:7
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Maso anga achita mdima chifukwa cha chisoni changa.+

      Maso anga akalamba chifukwa cha anthu onse ondichitira zoipa.+

  • Yesaya 59:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 Tikungoyenda ndi khoma ngati anthu akhungu, ndipo tikungofufuzafufuza ngati anthu opanda maso.+ Tapunthwa masanasana ngati kuti tili mu mdima wamadzulo. Pakati pa anthu ojintcha, tikungokhala ngati anthu akufa.+

  • Maliro 2:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Maso anga atopa ndi kulira.+ M’mimba mwanga mukubwadamuka.+

      Chiwindi changa chakhuthulidwa+ pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+

      Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda oyamwa akukomoka+ m’mabwalo a mzinda.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena